Utumiki wa Time of Repenting and Deliverance ku Domasi ukumanga sukulu ya Sekondare m’mudzi mwa Senior Group Namira mfumu yaikulu Mulilima ku Chikwawa.
Mkulu wa TIRDEM, mtumwi Albert Mpende watiuza kuti Utumikiwu wachita izi podziwa kuti maphunziro ndi ofunikira maka pa chitukuko cha dziko la Malawi.
Iye amayankhula izi Lolemba pa 24 March 2025 pomwe Nyungwe FM imafufuza mwachidwi zomwe zimamveka zoti Utumikiwu wayamba kumanga sukulu yoyambira makalasi a Form 1 mpaka 4.
Padakali pano ntchitoyi ili mkati ndipo ikadzatha sukuluyi idzatchedwa Guardian Christian Academy.
Wolemba: Jaison Chiyembekezo