Home Uncategorized SUKULU YOMWE UTUMIKI WA TIRDEM IKUMANGA IDZATCHULIDWA DZINA LOTI GUARDIAN CHRISTIAN ACADEMY

SUKULU YOMWE UTUMIKI WA TIRDEM IKUMANGA IDZATCHULIDWA DZINA LOTI GUARDIAN CHRISTIAN ACADEMY

by Robert Malenga
0 comments

Utumiki wa Time of Repenting and Deliverance ku Domasi ukumanga sukulu ya Sekondare m’mudzi mwa Senior Group Namira mfumu yaikulu Mulilima ku Chikwawa.

Mkulu wa TIRDEM, mtumwi Albert Mpende watiuza kuti Utumikiwu wachita izi podziwa kuti maphunziro ndi ofunikira maka pa chitukuko cha dziko la Malawi.

Iye amayankhula izi Lolemba pa 24 March 2025 pomwe Nyungwe FM imafufuza mwachidwi zomwe zimamveka zoti Utumikiwu wayamba kumanga sukulu yoyambira makalasi a Form 1 mpaka 4.

Padakali pano ntchitoyi ili mkati ndipo ikadzatha sukuluyi idzatchedwa Guardian Christian Academy.

Wolemba: Jaison Chiyembekezo

#Liwu_la_Mchigwa

You may also like

Leave a Comment

Nyungwe FM 107.6MHz is located near Thabwa Road Block in Chikwawa district.
Voice of the valley.

Newsletter

Subscribe my Newsletter for new blog posts, tips & new photos. Let's stay updated!

@2025 – All Right Reserved. MACRA Community Radios

Are you sure want to unlock this post?
Unlock left : 0
Are you sure want to cancel subscription?
-
00:00
00:00
Update Required Flash plugin
-
00:00
00:00