Mlangizi wa Zamaphunziro ku zone ya Boma m’boma la Chikwawa a Tobias Tembo ayamikira zomwe bungwe la Dyeratu Nzika lachita popereka mayunifolomu kwa ophunzira pa sukulu ya pulayimare ya Dyeratu m’bomali.

Nyungwe_FM_Nkhani

Poyankhula ku m’mawa wa Lolemba pa 17 March 2025 pa mwambo wopereka zovalazi, a Tembo apempha ophunzirawa kuti azigwiritse ntchito pa cholinga chake komanso kuchita khama pa maphunziro awo.

Mlembi wa gululi, a Francis Mazinga ati chidwi cha gululi ndi chofuna kufikira ophunzira ochuluka omwe ndi osowa m’madera a Katunga ndi Kasisi m’bomali.

Esther Lucius yemwe wapindula ndi thandizoli wati izi zamulimbikitsa pa maphunziro ake kuti adzakwaniritse khumbo lake lidzakhala mphunzitsi.

Asungwana khumi komanso anyamata khumi ndi asanu ndi omwe apatsidwa mayunifolomu ndi bungwe la Dyeratu Nzika.

Wolemba: Francis Mwale

#Liwu_la_Mchigwa

Related posts

Wailesi ya Nyungwe yakhazikitsa maere omwe pakutha pa tsiku anthu oposera makumi atatu azikhala akuchita mphumi yopambana ndalama yosachepera 10,000 kwacha

Boma la Malawi kudzera ku khonsolo ya boma la Chikwawa lakweza pantchito aphunzitsi a m’sukulu za pulayimale pafupifupi 900 a m’bomali.

Bungwe la center for human rights, Education,Advice and Assistance (CHREAA) lalangiza ophinzila achitsikana kuti azinena za nkhanza zogonana zomwe amakumanazo kwa adindo.