Home Uncategorized Mlangizi wa Zamaphunziro ku zone ya Boma m’boma la Chikwawa a Tobias Tembo ayamikira zomwe bungwe la Dyeratu Nzika lachita popereka mayunifolomu kwa ophunzira pa sukulu ya pulayimare ya Dyeratu m’bomali.

Mlangizi wa Zamaphunziro ku zone ya Boma m’boma la Chikwawa a Tobias Tembo ayamikira zomwe bungwe la Dyeratu Nzika lachita popereka mayunifolomu kwa ophunzira pa sukulu ya pulayimare ya Dyeratu m’bomali.

by Robert Malenga
0 comments

Nyungwe_FM_Nkhani

Poyankhula ku m’mawa wa Lolemba pa 17 March 2025 pa mwambo wopereka zovalazi, a Tembo apempha ophunzirawa kuti azigwiritse ntchito pa cholinga chake komanso kuchita khama pa maphunziro awo.

Mlembi wa gululi, a Francis Mazinga ati chidwi cha gululi ndi chofuna kufikira ophunzira ochuluka omwe ndi osowa m’madera a Katunga ndi Kasisi m’bomali.

Esther Lucius yemwe wapindula ndi thandizoli wati izi zamulimbikitsa pa maphunziro ake kuti adzakwaniritse khumbo lake lidzakhala mphunzitsi.

Asungwana khumi komanso anyamata khumi ndi asanu ndi omwe apatsidwa mayunifolomu ndi bungwe la Dyeratu Nzika.

Wolemba: Francis Mwale

#Liwu_la_Mchigwa

You may also like

Leave a Comment

Nyungwe FM 107.6MHz is located near Thabwa Road Block in Chikwawa district.
Voice of the valley.

Newsletter

Subscribe my Newsletter for new blog posts, tips & new photos. Let's stay updated!

@2025 – All Right Reserved. MACRA Community Radios

Are you sure want to unlock this post?
Unlock left : 0
Are you sure want to cancel subscription?
-
00:00
00:00
Update Required Flash plugin
-
00:00
00:00