Alimi a mzimbe okwana 762 ndi omwe atenga nawo mbali pa chisankhochi chomwe chinachitikira ku maofesi a zaulimi a Kasinthula pa msonkhano waukulu wa pa chaka wa alimiwa.
Wapampando wa Khonsolo ya m’bomali, a Martin Goche, womwe anali mlendo wolemekezeka alangiza adindo atsopanowa kuti aziyika zinthu poyera kuti alimi a mzimbe azipeza phindu lochuluka.
Atangosankhidwa pa udindowu, Amade Alide ati awonetsetsa kuti alimi akulandira ndalama zochuluka pa phindu lomwe amagawana kuti mabanja awo akhale otukuka.
Mlangizi wamkulu ku Unduna wa Zamalonda ndi Mafakitale, a Levi Longwe, apempha atsogoleri ongosankhidwa kuti azitsatira malamulo aboma oyendetsera magulu a zaulimi.
Pa chisankhochi, a Richard Mkomba asankhidwa kukhala wachiwiri kwa wapampando, a James Chiwambo apeza udindo wa mlembi ndipo wotsatira awo ndi a Stella Dzimwani pamene udindo wa msungichuma wapita kwa a Biyesi Chibowo.
Wolemba: Francis Mwale