Home Featured Magulu a alimi mzimbe a Kasinthula Can Growers Association m’boma la Chikwawa, pa 10 Epulo 2025 asankha Amade Alide kukhala wapampando wa alimiwa.

Magulu a alimi mzimbe a Kasinthula Can Growers Association m’boma la Chikwawa, pa 10 Epulo 2025 asankha Amade Alide kukhala wapampando wa alimiwa.

by Robert Malenga
0 comments

Alimi a mzimbe okwana 762 ndi omwe atenga nawo mbali pa chisankhochi chomwe chinachitikira ku maofesi a zaulimi a Kasinthula pa msonkhano waukulu wa pa chaka wa alimiwa.

Wapampando wa Khonsolo ya m’bomali, a Martin Goche, womwe anali mlendo wolemekezeka alangiza adindo atsopanowa kuti aziyika zinthu poyera kuti alimi a mzimbe azipeza phindu lochuluka.

Atangosankhidwa pa udindowu, Amade Alide ati awonetsetsa kuti alimi akulandira ndalama zochuluka pa phindu lomwe amagawana kuti mabanja awo akhale otukuka.

Mlangizi wamkulu ku Unduna wa Zamalonda ndi Mafakitale, a Levi Longwe, apempha atsogoleri ongosankhidwa kuti azitsatira malamulo aboma oyendetsera magulu a zaulimi.

Pa chisankhochi, a Richard Mkomba asankhidwa kukhala wachiwiri kwa wapampando, a James Chiwambo apeza udindo wa mlembi ndipo wotsatira awo ndi a Stella Dzimwani pamene udindo wa msungichuma wapita kwa a Biyesi Chibowo.

Wolemba: Francis Mwale

You may also like

Leave a Comment

Nyungwe FM 107.6MHz is located near Thabwa Road Block in Chikwawa district.
Voice of the valley.

Newsletter

Subscribe my Newsletter for new blog posts, tips & new photos. Let's stay updated!

@2025 – All Right Reserved. MACRA Community Radios

Are you sure want to unlock this post?
Unlock left : 0
Are you sure want to cancel subscription?
-
00:00
00:00
Update Required Flash plugin
-
00:00
00:00