Wachiwiri kwa mkulu wa bungweli, a Dorothy Kamtiza ati bungweli likugwira ntchito yosamalira zomera ndi nthaka komanso kubzala mbewu zakudimba ku sukulu zinayi pakupereka upangiri kwa ophunzira kuti akhale odzidalira.
A Kamtiza ayankhula izi Lachitatu pa 26 March 2025 pa sukulu ya sekondare ya Chang’ambika komwe bungwe la MAWO ndi ophunzira amagwira limodzi ntchito yosamalira zomera, mbewu ndi nthaka kudzera mu ntchito yomwe adayiyambitsa pa sukuluyi.
M’mawu ake, wophunzira wa pa sukuluyi Mercy Wright wati ophunzira amapeza ndiwo, kukolola madzi komanso ndalama kudzera mu ntchito yomwe amagwira pa sukulu yawo.
Bungwe la MAWO likugwira ntchitoyi ku sukulu ya sekondare ya Chang’ambika ndi zina zitatu za pulayimare za Changoima, Makandambidzi ndi Chutungwani m’dera la zamaphunziro la Changoima.
Wolemba: Francis Mwale
All reactions:
44