Home Uncategorized Bungwe la Maziko a Moyo Wabwino wa Onse (MAWO) lalimbikisa ntchito yosamalila zachilengedwe m’sukulu za pulayimare ndi sekondare za m’boma la chikwawa.

Bungwe la Maziko a Moyo Wabwino wa Onse (MAWO) lalimbikisa ntchito yosamalila zachilengedwe m’sukulu za pulayimare ndi sekondare za m’boma la chikwawa.

by Robert Malenga
0 comments

Wachiwiri kwa mkulu wa bungweli, a Dorothy Kamtiza ati bungweli likugwira ntchito yosamalira zomera ndi nthaka komanso kubzala mbewu zakudimba ku sukulu zinayi pakupereka upangiri kwa ophunzira kuti akhale odzidalira.

A Kamtiza ayankhula izi Lachitatu pa 26 March 2025 pa sukulu ya sekondare ya Chang’ambika komwe bungwe la MAWO ndi ophunzira amagwira limodzi ntchito yosamalira zomera, mbewu ndi nthaka kudzera mu ntchito yomwe adayiyambitsa pa sukuluyi.

M’mawu ake, wophunzira wa pa sukuluyi Mercy Wright wati ophunzira amapeza ndiwo, kukolola madzi komanso ndalama kudzera mu ntchito yomwe amagwira pa sukulu yawo.

Bungwe la MAWO likugwira ntchitoyi ku sukulu ya sekondare ya Chang’ambika ndi zina zitatu za pulayimare za Changoima, Makandambidzi ndi Chutungwani m’dera la zamaphunziro la Changoima.

Wolemba: Francis Mwale

#Liwu_la_Mchigwa

All reactions:

44

You may also like

Leave a Comment

Nyungwe FM 107.6MHz is located near Thabwa Road Block in Chikwawa district.
Voice of the valley.

Newsletter

Subscribe my Newsletter for new blog posts, tips & new photos. Let's stay updated!

@2025 – All Right Reserved. MACRA Community Radios

Are you sure want to unlock this post?
Unlock left : 0
Are you sure want to cancel subscription?
-
00:00
00:00
Update Required Flash plugin
-
00:00
00:00