UTM NDI YAMPHAMVU KU CHIGWA CHA SHIRE

Yemwe akuyimira chipani cha UTM ngati Phungu wa Nyumba ya Malamulo pakati Boma la Chikwawa pa chisankho cha pa 16 September pano, Godfrey Taonga Banda ati chipanichi tsopano chili ndi mphamvu ku Chigwa cha Mtsinje wa Shire.

Banda wayankhula izi Lachinayi pa 10 Epulo 2025 pakutha pa misonkhano yoimaima yomwe mtsogoleri wa chipanichi Dr Dalitso Kabambe anachititsa m’boma la Chikwawa komwe amafotokozera anthu mfundo zotukula maboma a Chikwawa ndi Nsanje.

Banda wati anthu akadzamusankha iye ngati phungu komanso Dr Kabambe ngati pulezidenti wa dziko, anthu a pakati pa Chikwawa adzapindula nawo ndalama zokwana K100 billion zomwe ati Boma la UTM lidzapereka ku Khonsolo ya bomali kuphatikizapo K500 billion yopita ku ulimi wa nthilira.

Wolemba: Francis Mwale