UNITRANS YAKHAZIKITA NJIRA ZOPEWERA NGOZI

Akuluakulu a Kampani ya UNITRANS achenjeza anthu kuti azikhala a tcheru pamene galimoto zawo zikuluzikulu zonyamula mzimbe zikudutsa m’misewu m’madera awo pofuna kupewa ngozi.

Mkulu woona Zaubale wa anthu akudera ndi kampaniyi ku Nchalo, a Simeon Butao anena izi Lachinayi pomwe kampaniyi ikuyembekezeka kuyamba ntchito yonyamula mzimbe ku minda Lamulungu lino pa 27 Epulo, 2025.

Iwo ati ndi mlandu kutchinga galimotozo pamene zikudutsa zitanyamula mzimbe ndi cholinga chofuna kusolola mzimbezo.

A Butao ati ngozi zambiri zimachitika kamba ka anthu ena omwe amazendewera ndi kutchingira galimoto zawo ndi cholinga chofuna kusolola mzimbe.

Kuwonjezera apo, iwo adandaula ndi kuchuluka kwa ngozi zomwe zimachitika kamba ka akabanza.

Pofuna kuthana ndi vutoli, iwo ati kampani yawo ikhala akupereka maphunziro apadera akayendwe kwabwino ka pa msewu ndi zovala zonyezimira kwa akabanzawa kuti ngozi za mtunduwu zisamachitike.

#Liwu_la_Mchigwa

All reactions:

77