Galimoto yonyamula katundu ya mtundu wa track panopa, yatseka msewu pa chipata cha malo ochitira chipikiseni cha apolisi pa Kamuzu Bridge m’boma la Chikwawa.
Woyendetsa galimotoyo a Ganert Nyirenda, wauza Nyungwe FM kuti ngoziyi yachitika galimotoyi italephera kukwera mtunda kamba kusokonekera kwa magiya zomwe zinachititsa kuti ibwerere m’mbuyo.
Galimototoyi yomwe nambala yake ndi NE4410 inanyamula matumba 600 a simenti yomwe imachokera ku Blantyre ndi kukatula kwa Ngabu.
Wolemba: Francis Mwale