Mphunzitsi wamkulu pa sukulu ya pulayimare ya Dyeratu m’boma la Chikwawa, a Dackford Jeremia ati sukuluyi ili pa vuto lopeza madzi aukhondo okwanira.
Poyankhula ndi Nyungwe FM Lolemba pa 17 March 2025, a Jeremia ati pampu ya madzi oyendera mphamvu ya dzuwa omwe bungwe la UNICEF lidayika pa sukuluyi idawonongeka zomwe zikuchititsa kuti ophunzira azilimbirana ndi anthu a midzi yoyandikira madzi a mjigo umodzi okhawo omwe uli pa sukuluyi.
“Tikupempha kwa onse amafuno abwino kuti atithandize kugula pampu ya tsopano, sukulu ili ndi ndalama zosaposera K600,000 zimene timafunako ena akufuna kwabwino atithandizire chifukwa pampuyi ili pafupifupi K3,000,000 kuti tigule ina yatsopano,” anatero a Jeremia.
Sukulu ya pulayimare ya Dyeratu ili mu dera la Zamaphunziro la Boma ndipo ili bdi chiwerengero cha ophunzira okwana 2,223.
Wolemba: Francis Mwale