Gulu la Dyeratu Nzika Lachisanu lidayitanitsa magulu a chitetezo chakumudzi a Community Policing Forum (CPF) pa zokambirana pa sukulu ya pulayimare ya Dyeratu zothandiza kupereka chitetezo chokhwima m’deralo.
Poyankhula pa zokambiranazi, Mkulu woona za ubale wabwino pakati pa apolisi ndi anthu akudera m’boma la Chikwawa, Assistant Superintendent Kingsley Mvuthe anati mkumanowu unali wofunika maka pa nthawi ino yomwe milandu ya zaupandu ndi umbava yakula kwambiri m’madera ozungulira tawuni ya Dyeratu.
“Mkumanowu unali wopambana chifukwa tsopano nzika ziyamba kuzindikira za udindo wawo pa chitetezo zomwe zichititse kuti apolisi tizigwira ntchito yawo motamandika,” anatero a Mvuthe.
Mlendo Wolemekezeka pa zokambiranazi anali Khansala wa dera la Bwabwali pakati pa Chikwawa, Gerald Bede yemwe anati akufuna kupanga Dyeratu kukhala dera lokomera onse.
“Ndiyesetsa kuchita zokambirana ndi makampani komanso mabungwe omwe akugwira ntchito zao kuno kuti awathandize a Police Forum ndi zipangizo monga zovala zonyezimira, nyale komanso ma wenzulo zogwirira ntchito pamene akupereka chitetezo,” anatero Khansala Bede.
M’mawu awo a Mfumu Lauji 2 kwa Mfumu yaikulu Katunga anati m’mudzi momwe muli chitetezo anthu ake amakhala mwa bata ndi mtendere kotero iwo ati agwira ntchito limodzi ndi apolisi pa ntchito yopereka chitetezo m’derali.
Apolisi adayambitsa magulu a Community Policing Forum (CPF) m’chaka cha 1997 pamene dziko la Malawi limasintha kagwiridwe ka ntchito za polisi.
Wolemba: Francis Mwale