Gulu la Dyeratu Nzika, Lachisanu pa 21 March 2025 lalandira maphunziro olimbikitsa nzika kutengapo mbali ndi kutsatira ndondomeko za zitukuko pa Khonsolo.
Bungwe la National Initiative for Civic Education (NICE) ku Chikwawa ndilo lidakonzera maphunzirowa nzika ndi magulu ena a achinyamata owalimbikitsa kutenga mbali yolondoloza ntchito za chitukuko zomwe khonsolo imakwaniritsa pogwiritsa ntchito ndalama za CDF, DDF ndi GESD.
Mlangizi wamkulu wa bungwe la NICE m’bomali, a Chiyembekezo Gwazayani ati Nzika za Dyeratu zili ndi udindo wa umwini oyang’anira ndi kuyitanitsa zitukuko komanso kupereka maganizo pa momwe ntchito za chitukuko zikuyendera kuti zikhale zokhazikika.
Mlembi wa gulu la Dyeratu Nzika, a Francis Mazinga ati maphunzirowa awatsekula m’maso ponena kuti ngati nzika za kudera achilimika polimbikitsa ndi kulondiloza ntchito za chitukuko zogwirika m’madera awo.
Bungwe la NICE Trust laperekanso maphunziro ngati omwewa kwa mabungwe omwe si aboma a m’bomali ndipo thandizo lake lachokera ku European Union (EU).