Mafumu kwa Mfumu yaikulu Mulilima m’boma la Chikwawa athokoza Mtsogoleri wakale wa dziko lino Dr Joyce Mtila Banda kamba kopereka chakudya kwa mabanja 300.
Thandizoli labwera kamba ka pempho lomwe Senior Group Namila adapereka kwa Dr Banda pa msonkhano womwe chipani cha People’s (PP) chidachititsa pa bwalo la Namila pa 1 March 2025 loti anthu kumeneko akuvutika ndi njala.
“Tili mu nthawi yomwe anthu ambiri akuvutika ndi njala choncho zomwe achita mayi Joyce Banda ndipemphe ena kuti atithandize,” anatero Mfumu Namila.
Pa tsikuli, Mtsogoleri wakale wa dziko linoyu adalonjeza zofikira anthuwa ndi chimanga pasadathe masiku ochuluka zomwe zapherezera Lachiwiri pa 25 March 2025.
Banja lililonse lopindula lalandira makilogalamu khumi a chimanga.