CHIPATALA CHA MAKHUWIRA CHILI PA CHIOPSEZO CHA MADZI OSEFUKIRA

Ogwira ntchito komanso odwala pa chipatala cha Makhuwira adandaula kuti amavutika ndi madzi omwe amasefukira mu Mtsinje wa Thelhiwani ponena kuti amasokoneza ntchito zaumoyo pa chipatalacho.

Kutsatira madandaulowa, Phungu wa Nyumba ya Malamulo Kumvuma kwa Chikwawa m’Chipani cha United Democratic Front (UDF), Wolemekezeka Rhodrick Khumbanyiwa, apempha Boma kudzera ku Unduna wazaumoyo kuti limange tchingo pa Mtsinje wa Thelhiwani omwe umasefukira pa chipatala cha Makhuwira.

“Ndikuthokoza kwambiri kuti chipatalacho chakuzidwa ndi Rural Community Hospital tsopano, koma ndi zimene zikuchitika pamenepo sizikukhala bwino n’chifukwa ndinayimirira mu Nyumba ya Malamulo kupempha zimenezo,” anatero Wolemekezeka Khumbanyiwa.

Ngakhale Phunguyu wakhala akuthandizapo pa vutoli pomanga tchingo longoyembekezera, vutoli likupitilira zomwe wati zikufunika Boma kulowererapo mwachangu kuti ntchito za umoyo zisamayimeyime kamba ka mavuto a madzi osefukira.

Mlangizi wa Zaumoyo pa chipatalacho, a Godfrey Malunga, awuza Nyungwe FM kuti madzi osefukira mu Mtsinje wa Thelhiwani amalowa m’zipinda zambiri za chipatalacho monga kuchidikiliro, koyezetsa matenda ndi kolandirira mankhwala mwa zina.

Kumbali yawo, Nyakwawa Mpangowalimba ya m’deralo, yathokoza phunguyu popereka masaka omwe adamangira tchingo la mchenga komabe nawo apempha Boma kuti liwamangire lina lolimba kuti chipatala cha Makhuwira ndi midzi yozungulira itetezeke ku madzi osefukirawa.

Chaka cha 2024 Boma lidakuza Chipatala cha Makhuwira ku East Bank kukhala m’gulu la zipatala zomwe zimatchedwa Rural Hospital.

#Liwu_la_Mchigwa

+2

All reactions:

9Esnart Najah McMillan and 8 others

Related posts

Wailesi ya Nyungwe yakhazikitsa maere omwe pakutha pa tsiku anthu oposera makumi atatu azikhala akuchita mphumi yopambana ndalama yosachepera 10,000 kwacha

Boma la Malawi kudzera ku khonsolo ya boma la Chikwawa lakweza pantchito aphunzitsi a m’sukulu za pulayimale pafupifupi 900 a m’bomali.

Bungwe la center for human rights, Education,Advice and Assistance (CHREAA) lalangiza ophinzila achitsikana kuti azinena za nkhanza zogonana zomwe amakumanazo kwa adindo.