Bungwe la Community Focus (COFO) Lachitatu pa 26 March 2025 lapereka zipangizo zophunzirira pa sukulu ya pulayimare ya Matchombe m’dera la zamaphunziro la Boma m’boma la Chikwawa.
Mkulu wa bungweli, a Joshua Malunga awuza wailesi ya Nyungwe kuti apereka ma yunifolomu komanso nsapato kwa ophunzira amasiye komanso ovutikitsitsa okwana 60.
A Malunga ati aperekanso mabuku, makopo ndi zolembera ndi cholinga choti maphunziro apite patsolo m’boma la Chikwawa.
Wolemba: Chifundo Bwalamba
Wojambula zithunzi: COFO
All reactions:
1414