Kwa Ngabu m’boma la Chikwawa, apolisi ati amanga mayi ena a zaka 27 kamba kotayira mwana wobereka wokha m’chimbudzi chokumba kamba koti mwamuna wake adakana pathupi pa mwanayo.
Mneneri wa apolisi m’bomali, Sergeant Dickson Matemba wati maiyu adapalamula mlanduwu pa 23 March 2025 m’mudzi mwa Thobwa kwa Mfumu yaikulu Ngabu m’bomali.
Padakali pano apolisi m’bomali omwe adzudzula mchitidwewu ati atengera maiyu ku bwalo la milandu ndi kukayankha pa mlandu womwe akumuganizira kuti wapalamula.
Wolemba: Francis Mwale