Ntchito yomanga malo osambira pa chipatala chaching’ono cha Chavala m’dera la Mfumu yaikulu Kasisi m’boma la Chikwawa yayamba Lolemba pa 17 March 2025
Malingana ndi amene wapereka thandizo la ntchitoyi, Patrick Kampira yemwenso ndi Shadow MP wa UTM Kumpoto kwa Chikwawa wati wachita izi pokhudzika ndi kuperewera kwa malo osambira pa chipatalachi.
Kampira wati ndi khumbo lake kuti akadzapambana pa chisankho cha pa 16 September 2025 kudzatukula ntchito za umoyo pa chipatalachi ndi zipatala zonse za Kumpoto kwa Chikwawa.
M’modzi mwa zzika za derali a Edwin Moda ayamikira zomwe Kampira wachita ponena kuti mavuto aukhondo pa chipatalachi tsopano achepa.
Wolemba: Jaison Chiyembekezo