Home Uncategorized Ntchito yomanga malo osambira pa chipatala chaching’ono cha Chavala m’dera la Mfumu yaikulu Kasisi m’boma la Chikwawa yayamba Lolemba pa 17 March 2025.

Ntchito yomanga malo osambira pa chipatala chaching’ono cha Chavala m’dera la Mfumu yaikulu Kasisi m’boma la Chikwawa yayamba Lolemba pa 17 March 2025.

by Robert Malenga
0 comments

#Nyungwe_FM_Nkhani

Ntchito yomanga malo osambira pa chipatala chaching’ono cha Chavala m’dera la Mfumu yaikulu Kasisi m’boma la Chikwawa yayamba Lolemba pa 17 March 2025

Malingana ndi amene wapereka thandizo la ntchitoyi, Patrick Kampira yemwenso ndi Shadow MP wa UTM Kumpoto kwa Chikwawa wati wachita izi pokhudzika ndi kuperewera kwa malo osambira pa chipatalachi.

Kampira wati ndi khumbo lake kuti akadzapambana pa chisankho cha pa 16 September 2025 kudzatukula ntchito za umoyo pa chipatalachi ndi zipatala zonse za Kumpoto kwa Chikwawa.

M’modzi mwa zzika za derali a Edwin Moda ayamikira zomwe Kampira wachita ponena kuti mavuto aukhondo pa chipatalachi tsopano achepa.

Wolemba: Jaison Chiyembekezo

#Liwu_la_Mchigwa

You may also like

Leave a Comment

Nyungwe FM 107.6MHz is located near Thabwa Road Block in Chikwawa district.
Voice of the valley.

Newsletter

Subscribe my Newsletter for new blog posts, tips & new photos. Let's stay updated!

@2025 – All Right Reserved. MACRA Community Radios

Are you sure want to unlock this post?
Unlock left : 0
Are you sure want to cancel subscription?
-
00:00
00:00
Update Required Flash plugin
-
00:00
00:00