Maerewa akhazikitsidwa lachitatu pa 21 may 2025 pamene wailesiyi yamaliza zokambilana zake ndi kampani yochititsa maere ya Supa win
Malingana ndi yemwe akuedetsa za maelewa M’modzi mwa ogwira ntchito kuchokera pa wailesi ya Nyungwe Robert Benson Malenga wati maelewa azitchulidwa kuti Nyungwe Supa win omwe kulowa kwake ndi kuimba *4348 * 26 # pa lamya ya mmanja
Kuonjezera apo omwe akutenga mbali yochita maelewa akuenera kukhala ndi ndalama yosachepera 500 kwacha Ku mpamba kapena Airtel money yomwe iziwathandizira kugura tikiti yolowera mu maelewa ndikukhala pa ndandanda wa anthu omwe azikhala akuchita mphumi nthawi iliyonse yomwe maelewa akuchitika.
Olemba Martha Chirwa M’biza
#Liwu la M’chigwa

All reactions:
10Moses Moyala and 9 others