wanena izi ndi modzi mwa akuluakulu ku bungweli,mayi Hope Gee Williams pa mwambo olimbikitsa ufulu wa anthu,womwe unachitikila pa sukulu ya sekondale ya St Michaels boma la chikwawa.
Mayi Williams ati bungweli lachita izi pozindikila kuti atsikana ambili amabisa za nkhanza zomwe amakumana nazo tsiku ndi tsiku.ndipo mayi Williams ati nkumanowu unali wofunika kwambili kamba kuti wathandizila kuzindikilitsa atsikanawa zakuyipa kwa ma ukwati awana achichepele.
Mayi Williams alangiza ophunzilawa kuti akhazikitse ma gulu oti azithandizana komanso kulimbikitsana pa nkhani ya zamaphunzilo
wolemba:Robert Benson Malenga