Kampani ya Illovo Sugar Malawi mogwirizana ndi bungwe la Catholic Relief Services (CRS) komanso Boma la Malawi, amanga nyumba zitatu zachitsanzo ku Nkombedzi, ku Nchalo m’boma la Chikwawa zomwe ndi zolimbana ndi kusitha kwa nyengo komanso zosalowa nthumba.
Mkulu woyang’anira ntchito ku kampani ya Illovo Sugar Malawi, a Kondwani Msimuko ati cholinga chawo ndi choti anthu azikaona nyumbazi kuti zifikire madera ena m’dziko muno.
M’mau ake Nduna yowona za Malo, a Deus Gumba ati Boma lachita chidwi ndi ntchitoyi ndipo lapanga ngwirizano ndi banki ya NBS ndi bungwe la NEEF kuti azipereka ngongole kwa Amalawi zomangira nyumba ngati izi.