Poyankhula ku m’mawa wa Lolemba pa 17 March 2025 pa mwambo wopereka zovalazi, a Tembo apempha ophunzirawa kuti azigwiritse ntchito pa cholinga chake komanso kuchita khama pa maphunziro awo.
Mlembi wa gululi, a Francis Mazinga ati chidwi cha gululi ndi chofuna kufikira ophunzira ochuluka omwe ndi osowa m’madera a Katunga ndi Kasisi m’bomali.
Esther Lucius yemwe wapindula ndi thandizoli wati izi zamulimbikitsa pa maphunziro ake kuti adzakwaniritse khumbo lake lidzakhala mphunzitsi.
Asungwana khumi komanso anyamata khumi ndi asanu ndi omwe apatsidwa mayunifolomu ndi bungwe la Dyeratu Nzika.
Wolemba: Francis Mwale